4 Mutibweze, Mulungu wa cipulumutso cathu,Nimuletse udani wanu wa pa ife.
5 Kodi mudzatikwiyira nthawi zonse?Kodi mudzakhala cikwiyire mibadwo mibadwo?
6 Kodi simudzatipatsanso moyo,Kuti anthu anu akondwerere ndi Inu?
7 Tionetseni cifundo canu, Yehova,Tipatseni cipulumutso canu.
8 Ndidzamva colankhula Mulungu Yehova;Pakuti adzalankhula zamtendere ndi anthu ace, ndi okondedwa ace;Koma asabwererenso kucita zapusa.
9 Indedi cipulumutso cace ciri pafupi ndi iwo akumuopa Iye;Kuti m'dziko mwathu mukhale ulemu.
10 Cifundo ndi coonadi zakomanizana;Cilungamo ndi mtendere zapsompsonana,