15 Odala anthu odziwa liu la lipenga;Ayenda m'kuunika kwa nkhope yanu, Yehova.
16 Akondwera m'dzina lanu tsiku lonse;Ndipo akwezeka m'cilungamo canu.
17 Popeza Inu ndinu ulemerero wa mphamvu yao;Ndipo potibvomereza Inu nyanga yathu idzakwezeka.
18 Pakuti cikopa cathu cifuma kwa Yehova;Ndi mfumuyathu kwa Woyera wa Israyeli.
19 Pamenepo munalankhula m'masompenya ndi okondedwa anu,Ndipo mudati, Ndasenza thandizo pa ciphona;Ndakweza wina wosankhika mwa anthu.
20 Ndapeza Davide mtumiki wanga;Ndamdzoza mafuta anga oyera.
21 Amene dzanja langa lidzakhazikika naye;Inde mkono wanga udzalimbitsa.