25 Ndipo ndidzaika dzanja lace panyanja,Ndi dzanja lamanja lace pamitsinje.
26 Iye adzandichula, ndi kuti, Inu ndinu Atate wanga,Mulungu wanga, ndi thanthwe la cipulumutso canga.
27 Inde ndidzamuyesa mwana wanga woyamba,Womveka wa mafumu a pa dziko lapansi.
28 Ndidzamsungira cifundo canga ku nthawi yonse,Ndipo cipangano canga cidzalimbika pa iye.
29 Ndidzakhalitsanso mbeu yace cikhalire,Ndi mpando wacifumu wace ngati masiku a m'mwamba.
30 Ana ace akataya cilamulo canga,Osayenda m'maweruzo anga:
31 Nakaipsa malembo anga;Osasunga malamulo anga;