26 Iye adzandichula, ndi kuti, Inu ndinu Atate wanga,Mulungu wanga, ndi thanthwe la cipulumutso canga.
27 Inde ndidzamuyesa mwana wanga woyamba,Womveka wa mafumu a pa dziko lapansi.
28 Ndidzamsungira cifundo canga ku nthawi yonse,Ndipo cipangano canga cidzalimbika pa iye.
29 Ndidzakhalitsanso mbeu yace cikhalire,Ndi mpando wacifumu wace ngati masiku a m'mwamba.
30 Ana ace akataya cilamulo canga,Osayenda m'maweruzo anga:
31 Nakaipsa malembo anga;Osasunga malamulo anga;
32 Pamenepo ndidzazonda zolakwa zao ndi ndodo,Ndi mphulupulu zao ndi mikwingwirima.