8 Munaika mphulupulu zathu pamaso panu,Ndi zoipa zathu zobisika pounikira nkhope yanu.
9 Pakuti masiku athu onse apitirira m'ukali wanu;Titsiriza moyo wathu ngati lingaliro.
10 Masiku a zaka zathu ndiwo zaka makumi asanu ndi awiri,Kapena tikakhala nayo mphamvudi zaka makumi asanu ndi atatu;Koma teronso kukula kwao kumati cibvuto ndi copanda pace;Pakuti kumapitako msanga ndipo tithawa ife tomwe.
11 Adziwa mphamvu ya mkwiyo wanu ndani,Ndi ukali wanu monga ayenera kukuopani?
12 Mutidziwitse kuwerenga masiku athu motero,Kuti tikhale nao mtima wanzeru.
13 Bwerani, Yehova; kufikira liti?Ndipo alekeni atumiki anu.
14 Mutikhutitse naco cifundo canu m'mawa;Ndipo tidzapfuula mokondwera ndi kukondwera masiku athu onse.