1 Yehova acita ufumu; wadzibveka ndi ukulu;Wadzibveka Yehova, wadzimangirira mphamvu m'cuuno;Dziko lomwe lokhalamo anthu likhazikika, silidzagwedezeka.
2 Mpando wacifumu wanu ukhazikika kuyambira kale lija;Inu ndinu wosayambira ndi kale, lomwe.
3 Mitsinje ikweza, Yehova,Mitsinje ikweza mkokomo wao;Mitsinje ikweza mafunde ao.
4 Yehova Wam'mwamba ndiye wamphamvu,Wakuposa mkokomo wa madzi ambiri,Ndi mafunde olimba a nyanja.