4 Malo ozama a dziko lapansi ali m'dzanja lace;Cuma ca m'mapiri comwe ndi cace.
5 Nyanja ndi yace, anailenga;Ndipo manja ace anaumba dziko louma.
6 Tiyeni, tipembedze tiwerame;Tigwade pamaso pa Yehova, amene anatilenga:
7 Pakuti Iye ndiye Mulungu wathu,Ndipo ife ndife anthu a pabusa pace, ndi nkhosa za m'dzanja mwace.Lero, mukamva mau acel
8 Musaumitse mitima yanu, ngati ku Meriba,Ngati tsiku la ku Masa m'cipululu;
9 Pamene makolo anu anandisuntha,Anandiyesa, anapenyanso cocita Ine.
10 Zaka makumi anai mbadwo uwu unandimvetsa cisoni,Ndipo ndinati, Iwo ndiwo anthu osokerera mtima,Ndipo sadziwa njira zanga.