10 Nenani mwa amitundu, Yehova acita ufumu;Dziko lokhalamo anthu lomwe likhazikika kuti silingagwedezeke;Adzaweruza mitundu ya anthu molunjika.
11 Kumwamba kukondwere nilisekerere dziko lapansi;Nyanja ibume mwa kudzala kwace:
12 Munda ukondwerere ndi zonse ziri m'mwemo;Pamenepo mitengo yonse ya kunkhalango idzapfuula mokondwera;
13 Pamaso pa Yehova, pakuti akudza;Pakuti akudza kudzaweruza dziko lapansi:Adzaweruza dziko lokhalamo anthu ndi cilungamo,Ndi mitundu ya anthu ndi coonadi.