1 Yehova acita ufumu; dziko lapansi likondwere;Zisumbu zambiri zikondwerere.
2 Pomzinga pali mitambo ndi mdima;Cilungamo ndi ciweruzo ndizo zolimbitsa mpando wacifumu wace.
3 Moto umtsogolera,Nupsereza otsutsana naye pozungulirapo,
4 Mphezi zace zinaunikira dziko lokhalamo anthu;Dziko lapansi linaona nilinagwedezeka.
5 Mapiri anasungunuka ngati sera pamaso pa Yehova,Pamaso pa Ambuye wa dziko lonse lapansi.
6 Kumwamba kulalikira cilungamo cace,Ndipo mitundu yonse ya anthu ipenya ulemerero wace.