2 Yehova anawadziwitsira cipulumutso cace;Anaonetsera cilungamo cace pamaso pa amitundu.
3 Anakumbukila cifundo cace ndi cikhulupiriko cace ku nyumba ya Israyeli;Malekezero onse a dziko lapansi anaona cipulumutso ca Mulungu wathu.
4 Pfuulirani kwa Yehova, inu, dziko lonse lapansi;Kuwitsani ndi kupfuulira mokondwera; inde, yimbirani zomlemekeza.
5 Myimbireni Yehova zomlemekeza ndizeze;Ndi zeze ndi mau a salmo.
6 Pfuulani pamaso pa Mfumu Yehova,Ndi mbetete ndi liu la lipenga,
7 Nyanja Ipfuule ndi kudzala kwace;Dziko lokhalamo anthu ndi iwo okhalamo;
8 Mitsinje iombe manja;Mapiri apfuule pamodzi mokondwera;