5 Myimbireni Yehova zomlemekeza ndizeze;Ndi zeze ndi mau a salmo.
6 Pfuulani pamaso pa Mfumu Yehova,Ndi mbetete ndi liu la lipenga,
7 Nyanja Ipfuule ndi kudzala kwace;Dziko lokhalamo anthu ndi iwo okhalamo;
8 Mitsinje iombe manja;Mapiri apfuule pamodzi mokondwera;
9 Pamaso pa Yehova, popeza akudza kudzaweruza dziko lapansi;Adzaweruza dziko lokhalamo anthu ndi cilungamo,Ndi mitundu ya anthu molunjika,