1 Yehova ndiye mfumu; mitundu ya anthu injenjemere;Iye akhala pakati pa akerubi; dziko lapansi ligwedezeke.
2 Yehova ndiye wamkuru m'Ziyoni;Ndipo akwezeka pamwamba pa mitundu yonse ya anthu.
3 Alemekeze dzina lanu lalikuru ndi loopsa;Ili ndilo loyera.
4 Ndipo mphamvu ya mfumu ikonda ciweruzo;Inu mukhazikitsa zolunjika,Mucita ciweruzo ndi cilungamo m'Yakobo.
5 Mkwezeni Yehova Mulungu wathu,Ndipo padirani poponderapo mapasa ace:Iye ndiye Woyera.