6 Amene analenga zakumwamba ndi dziko lapansi,Nyanja ndi zonse ziri m'mwemo;Ndiye wakusunga coonadi kosatha:
7 Ndiye wakucitira ciweruzo osautsika;Ndiye wakupatsa anjala cakudya;Yehova amasula akaidi;
8 Yehova apenyetsa osaona;Yehova aongoletsa onse owerama;Yehova akonda olungama;
9 Yehova asunga alendo;Agwiriziza mwana wamasiye mkazi wamasiye;Koma akhotetsa njira ya oipa.
10 Yehova adzacita ufumu kosatha,Mulungu wako, Ziyoni, ku mibadwo mibadwo.Haleluya.