3 Likumbukile zopereka zako zonse,Lilandire nsembe yako yopsereza;
4 Likupatse ca mtima wako,Ndipo likwaniritse upo wako wonse.
5 Tidzapfuula mokondwera mwa cipulumutso canu,Ndipo m'dzina la Mulungu wathu tidzakweza mbendera:Yehova akwaniritse mapempho ako onse.
6 Tsopano ndidziwa kuti Yehova apulumutsa wodzozedwa wace;Adzambvomereza m'Mwamba mwace moyeraNdi mphamvu ya cipulumutso ca dzanja lace lamanja.
7 Ena atama magareca, ndi ena akavalo:Koma ife tidzachula dzina la Yehova Mulungu wathu.
8 Iwowa anagonieka, nagwa:Koma ife tauka, ndipo takhala ciriri.
9 Yehova, pulumutsani,Mfumuyo atibvomereze tsiku lakuitana ife.