3 Lingakhale gulu la ankhondo limanga misasa kuti andithyole,Mtima wanga sungacite mantha:Ingakhale nkhondo ikandiukira,Nde pomweponso ndidzakhulupira,
4 Cinthu cimodzi ndinacipempha kwa Yehova, ndidzacilondola ici:Kuti ndikhalitse m'nyumba ya Yehova masiku onse a moyo wanga,Kupenya kukongola kwace kwa Yehova ndi kufunsitsa m'Kacisi wace.
5 Cifukwa kuti pa dzuwa la tsoka Iye adzandibisa mumsasa mwace:Adzandibisa m'tsenjezi mwa cihema cace;Pathanthwe adzandikweza.
6 Ndipo tsopano mutu wanga udzakwezeka pamwamba pa adani anga akundizinga;Ndipo ndidzapereka m'cihema mwace nsembe za kupfuula mokondwera;Ndidzayimba, inde, ndidzayimbira Yehova zomlemekeza.
7 Imvani, Yehova, liu langa popfuula ine:Mundicitirenso cifundo ndipo mundibvomereze.
8 Pamene munati, Punani nkhope yanga; mtima wanga unati kwa Inu:Nkhope yanu, Yehova, ndidzaifuna.
9 Musandibisire ine nkhope yanu;Musacotse kapolo wanu ndi kukwiya:Inu munakhala thandizo langa;Musanditaye, ndipo musandisiye Mulungu wa cipulumutso canga,