1 Wodala munthuyo wokhululukidwa chimo lace;Wokwiriridwa coipa cace.
2 Wodala munthuyu Yehova samwerengera mphulupulu zace;Ndimo mumzimu mwace mulibe cinyengo.
3 Pamene ndinakhala cete mafupa anga anakalambaNdi kubuula kwanga tsiku lonse.
4 Cifukwa usana ndi usiku dzanja lanu linandilemera ine;Uwisi wanga unasandulika kuuma kwa malimwe.
5 Ndinabvomera coipa canga kwa Inu;Ndipo mphulupulu yanga sindinaibisa.Ndinati, Ndidzaululira Yehova macimo anga;Ndipo munakhululukira coipa ca kulakwa kwanga.