24 Mundiweruze monga mwa cilungamo canu, Yehova Mulungu wanga;Ndipo asandisekerere ine.
25 Asanene mumtima mwao, Hede, momwemo!Asanene, Tammeza iye.
26 Acite manyazi, nadodome iwo akukondwera cifukwa ca coipa cidandigwera:Abvekeke ndi manyazi ndi kupunzika iwo akudzikuza pa ine.
27 Apfuule mokondwera nasangalale iwo akukondwera naco cilungamo canga:Ndipo anene kosalekeza, Abuke Yehova,Amene akondwera ndi mtendere wa mtumiki wace.
28 Ndipo lilime langa lilalikire cilungamo canu,Ndi lemekezo lanu tsiku lonse.