1 Yehova, musandidzudzule ndi mkwiyo wanu:Ndipo musandilange moopsa m'mtima mwanu.
2 Pakuti mibvi yanu yandilowa,Ndi dzanja lanu landigwera.
3 Mumnofu mwanga mulibe camoyo cifukwa ca ukali wanu;Ndipo m'mafupa anga simuzizira, cifukwa ca colakwa canga.
4 Pakuti mphulupulu zanga zapitirira pamutu panga:Ndathodwa nazo monga ndi katundu wolemera.
5 Mabala anga anunkha, adaola, Cifukwa ca kupusa kwanga.