1 Ndinati, Ndidzasunga njira zanga,Kuti ndingacimwe ndi lilime langa:Ndidzasunga pakamwa panga ndi cam'kamwa,Pokhala woipa ali pamaso panga.
2 Ndinatonthola osanena mau, ndinakhala cete osalawa cokoma;Ndipo cisoni canga cinabuka.
3 Mtima wanga unatentha m'kati mwaine;Unayaka moto pakulingirira ine:Pamenepo ndinalankhula ndi lilime langa:
4 Yehova, mundidziwitse cimariziro canga,Ndi mawerengedwe a masiku anga ndi angati;Ndidziwe malekezero anga,
5 Onani, munaika masiku anga akhale monga kuyesa dzanja;Ndipo zaka zanga ziri ngati cabe pamaso panu:Indedi munthu ali yense angakhale wokhazikika, ali cabe konse.
6 Indedi munthu ayenda ngati mthunzi:Indedi abvutika cabe:Asonkhanitsa cuma, ndipo sadziwa adzacilandira ndani?