1 Monga nswala ipuma wefuwefu kukhumba mitsinje;Motero moyo wanga upuma wefuwefu kukhumba Inu, Mulungu.
2 Moyo wanga uli ndi ludzu la kwa Mulungu, la kwa Mulungu wamoyo:Ndikadze liti kuoneka pamaso pa Mulungu?
3 Misozi yanga yakhalangati cakudya canga,Usana ndi usiku;Pakunena iwo kwa ine dzuwa lonse,Mulungu wako ali kuti?
4 Ndizikumbukila izi ndipo nditsanulira moyo wanga m'kati mwa ine,Pakuti ndidafopita ndi unyinji wa anthu,Ndinawatsogolera ku nyumba ya Mulungu, ndi mau akuyimbitsa ndi kuyamika,Ndi unyinji wakusunga dzuwa lokondwera.
5 Udziweramiranji moyo wanga iwe?Ndi kuzingwa m'kati mwanga?Yembekeza Mulungu, pakuti ndidzamyamikansoCifukwa ca cipulumutso ca nkhope yace.