3 M'mawa, Yehova, mudzamva mau anga;M'mawa, ndidzakukonzerani pemphero langa, ndipo ndidzadikira.
4 Pakuti Inu sindinu Mulungu wakukondwera naco coipaMphulupulu siikhala ndi Inu.
5 Opusa sadzakhazikika pamaso panu:Mudana nao onse akucita zopanda pace.
6 Mudzaononga iwo akunena bodza:Munthu wokhetsa mwazi ndi wacinyengo, Yehova anyansidwa naye.
7 Koma ine, mwa kucuruka kwa cifundo canu ndidzalowa m'nyumba yanu:Ndidzagwada kuyang'ana Kacisi wanu woyera ndi kuopa Inu.
8 Yehova, munditsogolere m'cilungamo canu, cifukwa ca akundizondawo;Mulungamitse njira yanu pamaso panga.
9 Pakuti m'kamwa mwao mulibe mau okhazikika;M'kati mwao m'mosakaza;M'mero mwao ndi manda apululu:Lilime lao asyasyalika nalo.