5 Mukwezeke m'mwambamwa mba, Mulungu;Ulemerero wanu ukhale pamwamba pa dziko lonse lapansi.
6 Anandichera ukonde apo ndiyenda;Moyo wanga wawerama:Anandikumbira mbuna patsogolo panga;Anagwa m'kati mwace iwo okha.
7 Mtima wanga wakhazikika, Mulungu, ndakhazika mtima;Ndidzayimba, inde, ndidzayimba zolemekeza.
8 Galamuka, ulemu wanga; galamukani cisakasa ndi zeze:Ndidzauka ndekha mamawa.
9 Ndidzakuyamikirani mwa anthu, Ambuye:Ndidzakuyimbirani mwa mitundu.
10 Pakuti cifundo canu ncacikuru kufikira m'mwamba,Ndi coonadi canu kufikira mitambo.
11 Kwezekani m'mwambamwamba, Mulungu;Ulemerero wanu ukhale pamwamba m'dziko lonse lapansi.