10 Mulungu wa cifundo canga adzandikumika:Adzandionetsa tsoka la adani anga.
11 Musawapheretu, angaiwale anthu anga:Muwabalalitse mwa mphamvu yanu, ndipo muwagwetse,Ambuye, ndinu cikopa cathu.
12 Pakamwa pao acimwa ndi mau onse a pa milomo yao,Potero akodwe m'kudzitamandira kwao,Ndiponso cifukwa ca kutemberera ndi bodza azilankhula.
13 Muwathe mumkwiyo, muwagurule psiti:Ndipo adziwe kuti Mulungu ndiye woweruza m'Yakobo,Kufikira malekezero a dziko la pansi.
14 Ndipo abwere madzulo, auwe ngati garu,Nazungulire mudzi.
15 Ayendeyende ndi kufuna cakudya,Nacezere osakhuta.
16 Koma ine, ndidzayimbira mphamvu yanu;Inde ndidzayimbitsa cifundo canu mamawa:Pakuti Inu mwakhala msanje wanga,Ndi pothawirapo ine tsiku la nsautso yanga.