11 Mboni za ciwawa ziuka,Zindifunsa zosadziwa ine.
12 Andibwezera coipa m'malo mwa cokoma,Inde, asaukitsa moyo wanga.
13 Koma ine, pakudwala iwowa, cobvala canga ndi ciguduli:Ndinazunza moyo wanga ndi kusala;Ndipo pemphero langa linabwera ku cifuwa canga.
14 Ndakhala ine monga ngad iye anali bwenzi langa, kapena mbale wanga:Polira ndinaweramira pansi, monga munthu wakulira maliro amai wace.
15 Ndipo pakutsimphina ine anakondwera, nasonkhana pamodzi:Akundipanda anandisonkhanira; ndipo sindinacidziwa:Ananding'amba osaleka:
16 Pakati pa onyodola pamadyerero,Anandikukutira mano.
17 Ambuye, mudzapenyerabe nthawi yanji?Bwezani moyo wanga kwa zakundiononga zao,Wanga wa wokha kwa misona ya mkango.