1 Mundicitire cifundo, Mulungu, mundicitire cifundo;Pakuti moyo wanga ukhulupirira Inu:Ndipo ndithawira ku mthunzi wa mapiko anu,Kufikira zosakazazo zidzapita.
2 Ndidzapfuulira kwa Mulungu Wam'mwambamwamba;Ndiye Mulungu wonditsirizira zonse.
3 Adzanditumizira m'mwamba, nadzandipulumutsaPonditonza wofuna kundimeza;Mulungu adzatumiza cifundo cace ndi coonadi cace.
4 Moyo wanga uli pakati pa mikango;Ndigona pakati pa oyaka moto,Ndiwo ana a anthu amene mano ao ali nthungo ndi mibvi,Ndipo lilime lao ndilio lupanga lakuthwa.
5 Mukwezeke m'mwambamwa mba, Mulungu;Ulemerero wanu ukhale pamwamba pa dziko lonse lapansi.
6 Anandichera ukonde apo ndiyenda;Moyo wanga wawerama:Anandikumbira mbuna patsogolo panga;Anagwa m'kati mwace iwo okha.