2 Ndidzapfuulira kwa Mulungu Wam'mwambamwamba;Ndiye Mulungu wonditsirizira zonse.
3 Adzanditumizira m'mwamba, nadzandipulumutsaPonditonza wofuna kundimeza;Mulungu adzatumiza cifundo cace ndi coonadi cace.
4 Moyo wanga uli pakati pa mikango;Ndigona pakati pa oyaka moto,Ndiwo ana a anthu amene mano ao ali nthungo ndi mibvi,Ndipo lilime lao ndilio lupanga lakuthwa.
5 Mukwezeke m'mwambamwa mba, Mulungu;Ulemerero wanu ukhale pamwamba pa dziko lonse lapansi.
6 Anandichera ukonde apo ndiyenda;Moyo wanga wawerama:Anandikumbira mbuna patsogolo panga;Anagwa m'kati mwace iwo okha.
7 Mtima wanga wakhazikika, Mulungu, ndakhazika mtima;Ndidzayimba, inde, ndidzayimba zolemekeza.
8 Galamuka, ulemu wanga; galamukani cisakasa ndi zeze:Ndidzauka ndekha mamawa.